You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma07/06/15

07/06/15

Written by  Newsroom

Azimayi atatu awilikiza uhule
Anthu aku Mbayani mu mzinda wa Blantyre akuti aimika manja m’mwamba chifukwa cha zomwe amai atatu apa banja akuchita powilikiza za uhule ndi amuna apa banjanso.

10
June

Panopa, mabanja a akaziwo ali teketeke chifukwa cha nkhaniyi. Chomwe chikudabwitsa anthu nchakuti amai-wo akumaputa dala amuna makamaka amene ali pabanja koma ofewetsa manja. Masiku angapo apitawa, mmodzi mwa amaiwo adamupezelela akuchita chisembwere ndi mwamuna wa mwini ku nyumba ina yogona anthu apa ulendo ku Mbayani komweko. Panopa nkhani ya mai-yo yawanda kwambiri mderalo koma mwamuna wake palibe chomwe chikumukhudza chifukwa kwa Iye zonse zili myaaa. Amuna a akazi enawonso salabadira akawauza kuti akazi awo awirikiza kuchita chiwerewere ndi amuna a eni ndipo zikumveka kuti amunawa anawapha mitima powadyetsa khuzumule.

 

Njoka iluma chala
Mamuna wina waopsyeza kuti aponda mwa asing’anga kuti akaunikile chomwe chachitika kuti njoka yosadziwika bwino ilume mnyamata wake chala kumunda pamudzi wina kwa Ngabu m’boma la Chikwawa. Nkhaniyi ikuti kutacha m’mawa, mkuluyo anadzutsa ana ake kupita nawo kukalima kudimba ndipo ali pa ndime mmodzi mwa anyamatawo njoka inamuluma mosadziwika bwino. Bamboyo pamenepa anathamangila komweko atamva kulila kwa mnyamatayo ndipo atafika pa malowo panalibe chilombo chomwe anachiona. Koma mnyamatayo anauza atate akewo kuti njoka inamuluma ndipo bamboyo akukhulupilila kuti ndiya matsenga. Mwanayo anamtengela ku mankhwala ndipo kumeneko ng’anga inamuuza kuti mai aakulu a mnyamatayo ndi omwe anatumiza njokayo m’matsenga.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter