You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma11/10/17

11/10/17

Written by  Newsroom

Mkulu wina wathawa pa mudzi kamba ka mantha

Mkulu wina wa m’mudzi mwa Malembe m’dera la Mfumu Chitukula mboma la Lilongwe wathawa m’mudzimo poopa anthu olusa omwe adamumenya kwambili mpaka kufuna kumupha pomuganizira kuti ndi mfiti.

11
October

Chomwe chinachitika nchoti mwana wa chaka ndi theka wa banja lina m’mudzimo amasewera ndi anzake koma kenaka anasowa mosadziwika bwino. Patatha masiku asanu mwanayo anapezeka m’chimbudzi akuyandama. Malinga ndi momwe adasowera mwanayo, anthu ambili amaganiza kuti izi zidachitika m’matsenga ndipo amaganizira mkuluyo. Apa anthuwo anayamba kumumenya mkuluyo molapitsa koma mwa mwayi achitetezo m’mudzimo anamulanditsa kwa anthu okwiyawo. Malinga ndi mkuluyo, akuti mwanayo anagwera mchimbudzicho chifukwa choti chinali chogumuka mbali imodzi komanso anawo anali okhaokha pakhomopo opanda wamkulu owayang’anira. Koma makolo a mwanayo atapita kwa sing’nga wa mizimu komanso Mneneri wina, anawatsimikizira kuti mkuluyo ndiye adasowetsa mwanayo m’matsenga. Pakadali pano mkuluyo wati alibenso maganizo obwerera kwawoko malinga ndi zomwe adazionazo.

Mwamuna wina amenya mkazi wake kamba ka foni
Mwamuna wina kwa mfumu Chigalu mboma la Blantyre wamenya kwambili bwenzi lake atamupeza ndi foni yapamwamba. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anapita kumudzi kwa bwenzi lakelo kukakhala nawo pa mwambo wa chiliza. Atalowa m’nyumba anapeza foni yapamwamba kwambili ndipo atamufunsa za foniyo analephera kufotokoza zogwira mtima. Izi zinapsyetsa mtima mwamunayo mpaka anayamba kumuthidzimula. Anthu atamva phokosolo anathamangirako ndipo atamva nkhani yonse anamufunsisitsa kuti afotokoze komwe kunachokera foniyo komabe sizinathandize mpaka mwana wina ndiye anaulula kuti foniyo inali ya nzake wa mayiyo yemwe anaguliridwa ndi chibwenzi ndipo anamusungitsa nzakeyo poopa mwamuna wake. Mwanayo anatinso mayiyo akunamiza mwamuna wake kuti akuchita ganyu yomweta udzu kwa nzakeyo ncholinga choti akalandira ndalama akagule foni yapamwamba. Apatu mpamene anthu anadziwa kuti mtsikanyo amayendetsa chibwenzi cha nzake wapa banjayo zomwenso zakkhumudwitsa bwenzi lakelo kwambili. Pakadali pano banja la nzakeyo lasokonekera ndipo mwamuwa wachibwenziyo wayamba wadula phazi kumudziko.

 

Asamba magazi kamba ka umbava

Mnyamata wina mu mzinda wa Lilongwe wasamba magazi kamba ka umbava. Malinga ndi mtolankhani wathu yemwe anaona izi zikuchitika, mnyamatayo anali mmodzi mwa anthu omwe anali pa malo ena achisangalalo ku Bwandiro. Ndipo momwe zikhalira anthu osiyana-siyana anafika pamalopo kudzasangalala. Kupatula anthu oyenda pansi ena mwa iwo anafika pamolowo pa galimoto za hayala ndi ena anakwera galimoto zao. Ena mwa anthu omwe anafika pamalo achisangalalowo anali anyamata ena atatu. Atafika pamalowo analowa mu bala ina momwe adaitanitsa mowa ndipo anasiya makiyi kuphatikizapo kiyi wamotokala yawo pa kauntala kwinaku nkumatsitsira. Mosakhalitsa makiyi aja anasowa mosadziwika bwino. Koma anyamata ena anakaikra mmodzi mwa ena omwe anafikanso pamalopo. Apo eni makiwo atadziwitsa achitetezo apamalowo zakusowa kwa makiyiwo anayamba kusakasaka mnyamatayo ndipo adamupona ali ndi gulu lina la mbava zinzake zomwe zinalinso pamalowo. Koma mnyamatayo atadzindikira kuti akumusaka iye anapatsira makiwo mzake. Mwatsoka eni makiyi adamuona tsizinamtoleyo akupatsira mzake makiyiwo. Apo pamodzi ndi azachitetezowo anagwira mbavayo ndikuyamba kumuthibula mpaka kumusiya ali magazi okha-okha. Anthu omwe akumudziwa mnyamatayo ati ndi khalidwe lake lotola-tola koma iyo andaula kuti eni makiyiwo alakwa polanga okha mbavayo.


Achita zachisembwere mu bus yokufa
Anthu ochita malonda ku msika wina mu mzinda wa Mzuzu ati atopa ndi mchitidwe wa chisembwere womwe anthu ena akumachitira m’basi ina yomwe idafera pamalowo. Yemwe watumiza nkhanizi wati pamsikawo pali basi yomwe inafera pamalowo. Koma kamba kuti eni wake sanaikonzebe basiyo yomwe yakhalitsa pamalopo tsopano yasanduka chipinda chochitirano zadama. Mwa zina magalasi basiyo ngosaonekera mkati, aja amati a tinted komanso pamalopo palibe mlonda. Izi zapereka mpata kwa anthu ena omwe akumagwilitsa ntchito basiyo ngati malo ozithandizira akafuna kuchita zachisembwere. Pakadali pano anthu ena ochita malonda pamsikawo ati akatula nkhaniyi kwa akulu-akulu kuti achotse basiyo pamalopo kamba izi zikulimbikitsa mchitidwe wosakhulupilika kwa anthu ena ochita malonda. Nkhaniyi yazizizlitsa nkhongono anthu ena maka akulu akulu azipembezo omwenso amachitsa misonkhano yamapemphero. Iwo ati posakhalitsapa achititsa msonkhano wachitsitsimutso pa msikawo pofuna kuti Mulungu alowererepo kuthetsa zamanyazi zomwe zikuchitka pamalowa.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter