You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
03
June

03/06/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3560 times

Anjatidwa kamba kochita chisembwere ndi mkazi wa mwini
Mwamuna wina wa zaka 75 wapa mudzi wina m’boma la Thyolo akupika jere ya chaka chimodzi khothi la Majistrate m’bomalo litamupeza wolakwa pa mlandu wovulaza mwini mkazi komanso kuchita chisembwere ndi mkazi wake.

02
June

02/06/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3056 times

Akazi apamitala akunthana kamba ka ufa
Akazi awiri a bambo wina ku Chigwele mu msinda wa Mzuzu akuti akuonana ndi diso la nkhwezule atatibulana koopsya mpaka kudulana chala chifukwa chokanganilana Ufa.

02
June

01/06/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3285 times

Chikwama chibwelera
Mkulu wina wapa Kawisa kwa Chowe mboma la Mangochi angoti kakasi kusowa mtengo wogwira chikwama chake chitabwerela mu mzinda wa Lilongwe. Chomwe chinachitika ndichoti mkuluyu amachokera ku Lilongwe kupita ku Mangochi ku mwambo wa chikwati. Koma atangotsika pa siteji yapa Mangochi Turn Off nthawi yomweyo panafika Mini- bus ziwiri yopita ku Mangochi ndi ku Lilongwe koma chifukwa cha chiphwirikiti mkuluyu sanaziwe mini bus yoti akwere. Pamenepa m’modzi mwa mnyamata oyitanila mini-bus anayamba kukokerana chikwamacho mpaka kuthamanga mkuyika m’mini bus yopita ku Lilongwe. Koma atakwera m’mini bus inayo ndipo akuyendela ku Ulongwe anaitanitsa chikwama chake kwa kondakitala kuti alipile popeza mchikwamamo munali ndalama yomwa 3-Hundred thousand kwacha. Pamenepa kondakitalayo anauza mkuluyo kuti sanakweze chikwama chake koma anaona m’modzi mwa anyamata akuyika chikwamacho m’mini bus yopita ku Lilongwe. Mkuluyo akuti analira ndikupempha dalaivala kuti abwerele popeza mchikwamamo munali ndal;ama zambiri. Izi zinachitika koma pamene amafika pa Sitejipo anapeza kuti galimotoyo yanyamuka ndipo chinyamata omwe amayitanila galimoto abalalika onse. Kenako mkuluyo anatsika mini-busyo uku akulira movetsa chisoni . Anthu ena akuloza chala achinyamata apa sitejiyo kuti akusowetsa mtendere kamba koti aka sikoyamba kuti katundu wa anthu asowe pa malopo.


Alira mokweza galu atafa
Mkulu wina ku Chingale m’boma la Zomba akuti anakuwa kwambiri ngati walandila uthenga wa maliro chikhalirecho amalilira galu wake amene wafa. Nkhaniyi ikuti mkuluyu anali ndi galu wake yemwe amamukonda kodabwitsa ndipo tsiku lina anapita ku Thondwe kukazonda matenda koma pobwera anapeza galu wake ali kwalaaa wafera pa Chigayo cha mkulu wina mderalo. Kenako mkuluyu anakakokela galuyo ndikumuyikha pa khonde. Pamenepa anthu ena anafika pakhomopo mkuluyu amangobindikira mnyumba uku akulira mokweza kuti galu wanga walakwanji ndipo ndikhala ndi ndani. Pakadali pano anthu ambiri akudabwa kuti ngati galuyo analidi galu weni-weni kapena anali galu wa masenga.

 

02
June

31/05/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3047 times

Azimayi avina motukula mitima yaazibambo pansika
Mabanja ena akuti atekeseka kwambili pamsika wa Mwazisi mboma la Rumphi amai anai oyendayenda atatulukila mkuyamba kuvina monyamula mitima ya amuna osiyanasiyana.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter