You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
02
June

30/05/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3077 times

Afuna kulanda nkhuku atalephera kupeleka k50
Kondakitala wina amudzudzula mpaka anthu ena okwela minibasi kufuna kumuphika zitadziwika kuti anafuna kulanda nkhuku mkulu wina atalephela kupeleka ndalama yokwana 50 kwacha kuti ikwanile pa ulendo wochokela ku Limbe kupita ku Blantyre.

02
June

29/05/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3028 times

Akunthana kodetsa nkhawa kamba ka ndudu yafodya
Anyamata awili akunthana kodetsa nkhawa mpaka kufuna kuchotsana mano polimbilana ndudu ya fodya pamudzi wa Mondiwa ku Bangwe mu mzinda womwewo wa Blantyre.

29
May

28/05/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3780 times


Mayi wina achita zodabwitsa nkachisi
Akhristu ampingo wina mtaunishipi ya Bangwe mu mzinda wa Blantyre aima mitu ndi zomwe anachita mai wina mkachisi atamaliza kulandila mgonelo.

29
May

27/05/15

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3814 times

Agwidwa ndi chibwenzi pa filling station

Mkulu wina anaona ngati malodza mkazi wake atamutukwana zamu nsalu pamene anamupeza ali ndi chibwenzi pa malo ena omwetsera mafuta ku Chilimba mu mzinda wa Blantyre.  Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali pa banja ndipo wakhala ndi mkazi wakeyo zaka zambili popanda kukayikilana kulikonse.  Ndiye  poti mtima wa nzako ndi tsidya lina, mayiyo wakhala akumva zoti mwamuna wakeyo ali ndi chibwenzi koma samakhulupilira mpang’ono pomwe. Patsikulo mayiyo amachokera ku Machinjiri ndipo ali m’minibus anaona galimoto ya mwamuna wakeyo ili pa Filling Station koma atayang’anitsitsa anaona kuti m’galimotomo muli mkazi yemwe pa nthawiyo amaseketsana naye mwachikondi. Posaugwira mtima  maiyo anapempha adalaivala kuti atsike koma mkazi wachibwenziyo atangomuona, anatuluka m’galimotomo nkuliyatsa liwiro kuthawa.  Anthu omwe anali pamalopo anayamba kumukuwiza koma akuti sanayang’ane m’mbuyo.  Apa mkuluyo anadziwiratu kuti yachimwa ndipo pofuna kuonetsa mtima wogonja anayitana mkazi wakeyo mwaulemu kuti akwere galimotoyo azikambirana momwemo. Koma chifukwa chopsya mtima maiyo anamutukwana mwamuna wakeyo zamu nsalu zomwe zinaoneka kuti mwamunayo sanayembekezere.  Mkuluyo anapitilizabe kupepesa mkazi wakeyo koma zinakanika moti aliyense anayenda ulendo wakewake.  Sizikudziwika kuti kunyumbako zinatha bwanji koma anthu ena omwe akuwadziwa anthuwo, ati banjalo  ndi lokondana kwambili ndipo nchachidziwikire kuti panopa anakhululukirana.

 

 

Agonana ndi bamboo ake omubeleka
Mtsikana wina akuyenda mogwetsa nkhope pansi mdela la makatani mu mzinda wa Lilongwe atamutulukila kuti wathetsa banja la mai ake chifukwa chochita zadama mdi bambo ake omubeleka. Nkhani-yi kwanthawi yaitali mtsikanayo wakhala akumachita zadama ndi bambo ake omubeleka. Koma mai ake akuti samakhulupilila nkhani-yi kufikila dzulo pamene anapezelela mtsikanayo akuchita zachisembwere ndi bambo ake. Pa chifukwa ichi, mai ake atuta katundu wao apita kwao kusiya mtsikanayo ndi bambo ake m’nyumbamo. Anthu ambili mdelalo akuti adzudzula zomwe mtsikanayo wachita ngakhale ati akukhulupilila kuti bamboyo chilipo chomwe akufuna kukhwimila mwana wake-yo. Malinga ndi amene watumiza nkhani-yi sizikudziwika kuti mai ndi mwana wakeyo azionana bwanji ngati onse atakumana kumudzi kwao.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter