You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma17/10/17

17/10/17

Written by  Newsroom

Amwalira atamwa mankhwala olemeletsa
Mwamuna wina wa zaka 22 wafa kwa Kachere mboma la Dedza atamwe mankhwala omwe sing’anga anamupatsa kuti alemela.

17
October

Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mkuluyo anapita ku Mozambique komwe anafuna mankhwala azitsamba kuti alemere. Sing’anga anamuuza mkuluyo kuti asade nkhawa koma kuti akakafika kunyumba akamwalila ndipo mkazi wake asakalile malilowo. Mwa zina anauza mnyamatayo kuti mkazi wake azikatolela mphutsi mkumaika m’matumba ndipo ikakatha sabata akauka ali khumutcha chifukwa mphutsizo zikakhala makwacha. Kufika kunyumba anamwadi mankhwala mpaka kumwalila. Mkazi wake anachita momwe anamuuzila pobisa thupilo mchipinda china. Koma masiku akumapita anthu anayamba kumva fungo loipa la chinthu chovunda ndipo atakaona anapeza kuti anali mwini nyumbayo. Nkhaniyo itapita ku polisi ya Njonja mogwilizana ndi achipatala ku Dedza anawalangiza kuti atha kukaika malilowo. Ku polisi mkaziyo anaulula zonse momwe zinachitikila mwamuna wakeyo. Pakadali pano, apolisi akulangiza anthu kuti apewe kunamizidwa ndi asing’anga kuti awapatsa mankhwala othandiza kuti alemere. Malemuyo amachokela pamudzi wa Chimowa kwa Kachere mboma lomwelo la Dedza.

 

Anthu apeza khanda mchimbudzi

Anthu a mmudzi mwa Chambwinja mfumu yaikulu Machinjiri mu mzinda wa Blantyre akufufuza mwini wa khanda lina lomwe lapezeka mchimbudzi china lero m’mawa. Malipoti akuti anthu ena omwe amadutsa pafupi ndi chimbudzi china anadabwa atamva kulira kwa mwana wakhanda mchimbudzi. Pamenepa, anthuwo anapita pa chimbudzicho pomwe anakapeza khandali likungolira. Zitatere anthuwa akuti anapita ku South Lunzu Police station komwe anapatsidwa kalata yomwe anapita nayo kuchipatala china mu mzindawu. Pakadali pano, ntchito ili mkati kufunafuna mai yemwe anataya nkhandalo lomwe akuganiza kuti latha masiku awili.

 

Alamulidwa kuti akumbe okha manda

Banja lina lakomana nazo mdera la Chadza ku Lilongwe nyakwawa ya mderalo italamula banjalo kuti lidzikumba lokha manda likaonekeredwa zovuta. Nkhaniyi ikuti banjalo kwa zaka zambiri lakhala lisakupita m’malilo kuphatikizapo kugona komanso kudya m’maliro. Akalifunsa limayankha m’maso muli gwa kuti anthuwo alibe mphamvu zowafunsa za nkhaniyi komanso ati amachita izi pa zifukwa za chipembedzo. Masiku apitawa m’modzi mwa anthu apa banjapo anamwalira ndipo pa mwambo wake uthenga unapita kwa nyakwawa ya mderalo. Apa nyakwawayo inauza adzukulu kuti tsiku lotsatila akakumbe manda ndipo adzukuluwo sanawilingule koma kusonkhano mwaunyinji kumandako. Chodabwitsa adzukuluwo amangocheza kumandako kufikira nthawi ya chakudya inakwana. Amai omwe anapititsa chakudya anagwira pakamwa ataona kuti mandawo sanakumbidwe komanso anakanitsitsa kudya chakudyacho. Uthenga unapita ku siwa ndipo nyakwawa ya mderalo inachonderela anthuwo kuti agwire ntchitoyo ndipo zinathekadi. Zonse zinatha mikoko yogona komanso anyakwawa ya mderalo analangiza anthuwo kuti alekeretu za khalidwe laolo apo abii akakumana ndi zovuta adzikumba okha.

 

Mwamuna wina asowa mtengo ogwira
Mwamuna wina mdera la Kalonga ku Salima manja ali ku nkhongo. Nkhaniyi ikuti mpondamatiki wina anatengana ndi mai wina oyendayenda ndikupita ku malo ogona anthu apa ulendo mderalo mcholinga choti akasangalale. Macheza atafika kumapeto maiyo anafunsa njondayo kuti amupatse ndalama zomwe anagwirizana koma mpondamatikiyo anayamba kutuluka thukuka atazindikira kuti pa nthawiyo analibe ndalama. Apa njondayo anapempha maiyo kuti amulore kuti alankhulane ndi mzake wina mcholinga choti amuthandize ndi ndalama yokwana 20-thousand yomwe maiyo amafuna pa nthawiyo. Koma maiyo posakhutila ndi zomwe imachita njondayo anangotenga makiyi a galimoto ndikuyamba kuthawa nawo zomwe zinapangitsa kuti mpondamatikiyo athamangitse maiyo ali ndi buluku lokha. Anthu apa malopo anayesa kuchonderela maiyo kuti amvetsetsane koma anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti abweza makiyi pokhapokha amupatse ndalamayo. Pamene timalandila nkhaniyi galimotolo likadali pa malopo ndipo sizikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji chifukwa mwa zina njondayo ikulephera kufika kunyumba pochita mantha ndi mkazi wake. Anthu ambiri mderalo ati asangalala ndi zomwe achita maiyo chifukwa mpondamatikiyo ndi khalidwe lake lokhalira kuyenda ndi akazi osiyana-siyana.

 

Katakwe wina awona polekera

Katakwe wina pa mangolomera ochokera mdziko la Mozambique omwe akukhala ku Migowi ku phalombe aona polekera. Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe amagulitsa njinga za moto mderalo wakhala akukhaulitsa amuna amzake mderalo powathambitsa ndi makofi podalira mangolomera omwe munthuyo anachekera ku Mozambique-ko. Tsiku lina mwamunayo ndeu ya fumbi inabuka pakati pa nzikayo ndi munthu wina pazifukwa zosadziwika bwino. Apa anthu omwe anali pa malopo ataona izi atakatsina khutu mikoko yogona yomwe inathamangira kunyumba kwa njondayo ndikuuza mkazi wake kuti awathandize. Mkaziyo sanavute koma kulowa mnyumba ndikukatsilikula chizimbacho. Izi zitachitika mwamunayo anathidzimulidwa ndi munthu winayo zomwe zinapangitsa kuti anthu akhulupilire za mangolomerawo. Nzikayo pakadali ayilipitsa chindapussa cha mbuzi ziwiri ndipo nyakwaw a ya mderalo yachenjeza kuti munthuyo akapitiliza ndi khalidwe lakelo amusamutsa mderalo. Paakadali pano katakweyo apepesa.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter