You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma01/07/15

01/07/15

Written by  Newsroom

Amuthamangitsa kubanja kamba kaumbombo
Bilidala wina ku Tsangano m’boma la Ntcheu akuyenda wela-wela ngati wataya singano mkazi wake atamuthamangitsa kuti sakumufuna banja kamba ka umbombo.

02
July

Mkuluyo anali pa banja ndi mkazi wa bizinesi yogulitsa phwetekere ndipo banja lawo limayenda bwino lomwe kotero kuti anthu ambiri amachita nalo kaso. Koma tsiku lina maiyo ankachokera ku geni yake yogulitsa tomato anadabwa kupeza bamboyo akunyoza ana owapeza a maiyo. Izi zinakwiitsa kwambiri mkaziyo yemwe sanachitire mwina koma nthawi yomweyo anapitikitsa mwamuma wa umbomboyo pa khomopo. Pakadalipano mwamunayo wagwira njakata chifukwa amadalira kwambiri mkaziyo ndi amenenso ali ndi mpamba wochuluka wa geni.

 

 

Afuna kupha mwana wawo kuti apeze chuma
Mamuna wina ku Lowonde m’boma la Machinga akuyenda monyowa kwambiri mkazi wake ataulula kuti akufuna kupha mwana wao kuti achitile chizimba choti apezele chuma. Banja-lo akuti lili ndi ana atatu ndipo limalima mbeu zosiyanasiyana zomwe limagulitsa. Koma masiku apita-wo awiri-wo anapita kwa sing’ang’a ati kukasaka chizimba choti apeze ndalama zambiri zoti ati agule minbus. Koma atafika ku nyumba mai-yo anasitha maganizo ndipo mmalo mochita zomwe sing’ang’a-yo ananena mai-yo akuti anayamba kuuza anthu ena za chizimba-cho. Pakadali pano nkhani-yi yafala kwambiri mdera-lo ndipo mwamunu wa mai-yo akuyenda mwa manyazi kwambiri pamene anthu-wo akukhalabe limodzi monga banja.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter