Mneneri wa apolisi m’boma la Dedza Edward Kabango wati mwamunayo Wilibesi Kafansiyanji wakhala akuzemberana ndi mwana wake wa mkaziyo potsatira chizimba cha mankhwala a zitsamba omwe adakatenga kwa sing’anga wina kumeneko kuti alemere. Mai a mtsikanayo kuphatikizapo mikoko yogona itampanikiza mtsikanayo anaulula m’maso muli gwa kuti pathupipo pomwe ndipa miyezi itatu ndipa atate ake. Nkhaniyi itaululika mwamunayo ananyamula dzingwe ndikukadzikhweza mu mtengo wa mango m’munda mwake. Ndipo malemuyo wasiya kalata yomwe ikuti amaopa kuti apolisi amumanga malinga ndi nkhaniyi.
Nsima isowa pasiwa
Mayi wina ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe anaseketsa anthu podandaulira anzake kuti msima yake yasowa pa siwa. Khaniyi ikuti mayiyo ndiwokangalika kukagwa zovuta mderalo, koma tsiku lina anapita ku maliro koma mwatsoka anapeza kuti mwambo wa maliro ukuyamba. Apa anapita ku miphika ya zakudya ndikumanga msika pa mpango ncholinga choti akabwerera kuchokera ku manda adzaone poyambila, koma osadziwa kuti adzukulu ena amaona zonse amachita mayoyo. Paja pali mau amati kumbuyo kuli maso adzukulu aja anaikhalira msima ija mpaka kumaliza, kumapeto kwake ndikumanga maduka a njerwa pa nsalupo. Mayiyo atafika anagofikira pa katundu wake koma mosazindikira anakasamba m’manja kuti adye chakudyacho. Koma anadzidzimuka kupeza kuti m’malo mopeza chakudya anapeza madukawo. Apa mayiyo anadandaulira amzake koma ena anamuthandiza ndi chakudya pamene ena amamuseka ndikumudzudzula kuti ku maliro sikosusukira zakudya koma kukathandiza anamfedwa.