You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma16/07/15

16/07/15

Written by  Newsroom

Amuumila mkazi kuti amuphe kamba ka mowa
Mikoko yogona yam’mudzi wina kwa Chakhaza mboma la Dowa yadzudzula mkulu wina yemwe amakonda kuti akaledzela adzisaka mkazi wake mpini wa khasu uli kumanja kuti ati amuphe.

16
July

Nkhaniyi ikuti mkulu wina ali ndi mkazi yemwe adabeleka naye ana asanu koma vuto ndi loti akaledzela sagwilika nkomwe chifukwa amalusa ngati nkhalamo. Mwa zina, mkuluyo akuti ali ndi chizolowezi chokonda kugulitsa chimanga akakolola ndipo ndalama zonse amapita kukamwela mowa. Tsono masiku apitawa zinthu zinafika povuta pamene mkuluyo anayamba kusaka mkazi wake mpini uli m’manja ati angomupha malinga nkuti amamuletsa kugulitsa chimanga chomwe anali nacho. Mkazi atathawa akuti anakabwela ndi akwao ndipo pamudzi ndi akuchimuna anagwilizana kuti banjalo lingosasuka mpaka awiliwo agawana katundu yense wa m’nyumba. Koma chomwe chikudabwitsa anthu mchakuti mwamunayo akuopsyeza kuti athana ndi mkaziyo pali ponse pomwe amupeze. Pa chifukwa ichi, akuchikazi ati akukonza zokanena ku polisi kuchitila pa m’mawa. Panopa, mkuluyo akuti wangosanduka chidole m’mudzimo malinga nkuti anthu akungomulozaloza.

 


Ayendetsedwa mbulanda kamba kachisembwere
Mkulu wina wakwa Kalumo mboma la Ntchisi, anamuyendetsa mbulanda kuzungulila mudzi atamupezelela akuchita zachisembwere ndi mkazi wamwini dzuwa likuswa mtengo. Nkhani-yi ikuti masiku apitawa mkulu wina anali pa chibwenzi ndi mkazi wina m’mudzimo chonsecho amadziwa kuti mkaziyo ali pabanja. Mbuyomo akuti anthu angapo akhala akumulangiza za nkhani-yi kuti azipewa mchitidwe wake wa mchiuno koma akuti amayankha mwathamo kuti ati samadeweza. Tsono paja amati tsiku la fote likakwana, tsiku lina mkuluyo akuti anagwilizana ndi mkazi wapa banja uja kuti akakumane pa thengo lina dzuwa likuswa mtengo. Ali kumeneko akuti anakolopola zovala zonse kuiwala zoti ati anali pathengo. Mosakhalitsa akucheza ndi mkaziyo anangoona amuna angapo akutulukila pamalopo ndipo m’modzi mwa amunawo anali mwini mkaziyo. Pamenepa, akuti analiyala liwilo kuthawa buluku lake lili m’manja koma amuna aja anakwanitsa kumugwila pamodzi ndi mkazi uja. Kenaka akuti anamufunsa ngati akufuna kumupaka chitedze ndikumuyendetsa mbulanda. Apa mkuluyo akuti anangoti ndwii kusowa choyankha ndipo amuna aja akuti anangoganiza zolowa naye m’mudzi ali buno bwamuswe kuzungulila naye mudzi. Anthu ena achifundo akuti ndi omwe anapepesa kuti amuveke zovala zake. Panopa, mkuluyo akubindikila m’nyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter