You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma04/07/15

04/07/15

Written by  Newsroom

Alandidwa katundu yense wa mnyumba
Anthu a kwa Mfumu Mnyanja m’boma la Kasungu anafa ndi chikhakhali mkulu wina yemwe amatsogolera kulanda anthu zinthu nayenso analandidwa katundu yense wa mnyumba.

07
July

Nkhaniyi ikuti mderalo anthu ambiri anatenga ngongole yochitila bizinezi kuchokera ku kampani ina yongongoza ndalama koma anagwirizana nthawi kuti ngati sakhala atabweza pa nthawi yomwe agwirizaneyo kampaniyo idzatenga katundu. Mwatsoka bizinezi zambiri sizinayende bwino mpaka nthawi inakwana. Pokhala kuti mkuluyo ali m’modzi mwa akuluakulu a gululo iye anatsogolera kampaniyo kulanda anzake katunduyo ngati njira imodzi yodzidzimbayitsa kuti amukhululukire. Anthu ambiri a gululo analandidwa katundu wa mnyumba wosiyanasiyana motsogozedwa ndi mkuluyo koma anthu ena anapita ku ufesi yayikulu ndikukaulura zachinyengo zomwe anthu ena anachita ndi mkuluyo. Tsiku lotsatila kunabwera anthu okwiya kudzalanda katundu yense wa mkuluyo, apa anthu anaseka mosalekeza ndipo anali osangalala kwambiri ndi zomwe zinachitikira mkuluyo. Akuluakulu ena omwe amayikira ku mbuyo mkuluyo ayamba awayimitsa ntchito.

 


Adzudzulidwa kamba kosayankhula bwino
Mwamuna wina kwa Kaomba m’boma la Kasungu wadzudzulidwa kwambiri kamba ka khalidwe lake losayankhula bwino ndi anthu. Nkhaniyi ikuti tsiku lina anthu a m’deralo anagwirizana kuti akalime ku manda monga mwa mwambo wake. Pobwerela ku manda kuja banja lili lonse linasonkhana ndikudya pomaliza pa ntchitoyo, koma bamboyo pokhala kuti analibe kalikonse anayamba kupempha anthu ena kuti amupase chakudya. Munthu woyamba kumupempha anakana ponena kuti chakudyacho sichikwanila, apa mamuna uja anakwiya kwambiri ndikuzazila mzakeyo ponena kuti ngwaumbombo komanso anapitiliza kunena kuti anthu aku banja kwake akamafa asamaike maliro pa mandawo. Apa mkuluyo anamukuwiza ndipo anachoka chozemba pa malopo, koma mafumu a mderalo ati ayitanitsa ku bwalo mkuluyo kuti amukhaulitse pa zomwe ananenazo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter