Nkhaniyi ikuti mkuluyo anakwatirana ndi mkazi wakeyo pakanthawi koma akuti Mayiyo amakhalira kulimba m’banjamo chifukwa cha khalidwe la mwamuna wakeyo lokonda akazi. Mayiyo wakhala akudzudzula mwamuna wakeyo paza khalidwe loipalo koma amangotayira malangizowo ku nkhongo. Masiku angapo apitawa mkuluyo akuti anaonjeza pomwe amalankhulana ndi zibwezi zakezo mkazi wakeyo ali pomwepo. Potopa ndi khalidweli mayiyo anatsomphola phone ya mwamuna wakeyo ndipo anamuuziratu kuti samupatsanso phone-yo. Mayiyo analamula mwamuna wakeyo kuti ali ndi ufulu kukadandaula kulikonse za nkhaniyi koma akuti mpaka pano mwamunayo sanakatule nkhaniyi kulikonse ngakhale kwa ankhoswe a banjalo. Chifukwa chpchita manyazi ndi nkhaniyi, mkuluyo akungobindikira m’nyumba poopa kuti anzake azimuseka.
Atukwana anthu kamba ka mowa
Anthu a m’mudzi wina m’dera la Mfumu Machinjiri mu mzinda wa Blantyre achenjeza kuti akhaulitsa mkulu wina ngati apitilize khalidwe lake lomatukwana anthu akamwa mowa. Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mkulu wina yemwe ndi mbiyang’ambe koma akuti ali ndi vuto lalikulu chifukwa akaledzera, anthu amamumvera patali, kutukwana aliyense m’mudzimo. Anthu ambiri m’mudzimo akhala akudandaula ndi khalidwe la mkuluyo yemwe akumuganizira kuti amachita kuchalira kutukwanako makamaka akasemphana maganizo ndi anthu ena m’deralo. Zikumvekanso kuti m’mbuyomu, mkuluyo anamuitanira ku bwalo la mfumu anthu ena atakadandaula za khalidwe lake loipalo koma m’malo mosintha, akungopitilizabe. Pachifukwachi gulu la anyamata ena mogwirizana ndi anthu okwiya ndi khalidweli achenjeza mkuluyo kuti akangopitiliza khalidwe lake lomatukwana anthu m’mudzimo awona chomwe chidameta nkhanga mpala.