Mayi otumbwa akunthidwa pa njigo
Mayi wina ku Nayuchi m’boma la Machinga wodziwika bwino ndi khalidwe lake lolalata komanso kudzimva waona polekera atakunthidwa kolapitsa ndi atsikana ena pa mjigo.
Alira ngati maliro mkazi atathesa ukwati
Mnyamata wina ku Chipoka m’boma la Salima wadabwitsa mikoko yogona atalira mokweza ati kamba koti mkazi wake wamusiya ukwati ati chifukwa choti mnyamatayo anaba chimanga cha apongozi ake.
Ndewu ibuka pakati pamabanja awiri
Ndeu yoopsya inabuka pakati pa mabanja awiri amene akukanganilana ufumu ku Thondwe m’boma la Zomba.
Agwetsedwa mu mpingo kamba kokanganilana mamuna
Amai awiri ampingo wina kwa Jenda m’boma la Mzimba awaimitsa mu mpingo atakhunthana koopsya chifukwa chokanganirana mwamuna.