You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
22
July

NSANJE IVUTA KU CHIKWAWA

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 345 times

Zomwe akuchita mkulu wina kwa Mgabu mboma la Chikwawa zikudabwitsa anthu pomwe akumachitira nsanje mkazi yemwe anasiyana naye ukwati. Nkhaniyi ikuti mkuluyo poyamba anakatenga mkazi ku Thyolo nkumakakhala naye kwawo monga mtengwa. Mayiyo akuti ndi wotakataka ndipo atapita ku Chikwawako anapitiliza geni yake yogulitsa kaunjika. Koma vuto nloti mwamunayo amaonjola ndalama za mayiyo akangozisiya poyera, ndipo izi zakhala zikumuwawa mayiyo maka chifukwa choti akamubera ndalamazo amakapatsa akazi ena. Potopa ndi khalidweli mayiyo anamuuza mwamunayo kuti akufuna akamutule kwawo koma mwamunayo amangonyalanyaza. Tsiku lina mwamunayo anafika ndi mkazi wina pakhomopo nkumuuza mkaziyo kuti achoke pakhomopo adzipita kwawo komwe akufunako. Mayiyo atamva izi, anangoti laponda la mphawi diwa, nthawi yomweyo kupakira katundu wake nkuona msana wa njira. Tsono mayiyo atasiyanitsa momwe geni ake imayendera mbomalo ndi kwawo ku Thyolo, anaganiza zochita lendi m’dera lomwelo.   Tsono chomwe chikumachitika panopa nchakuti, mwamunayo walemba aganyu woti azimulonda mayiyo moti anawauza kuti akandzangomuona mayiyo ndi mwamuna wina adzamudziwitse msanga. Koma anthu atamva nkhaniyi, adabwa nazo kwambili ati kaamba koti mwamunayo ndiye anamuthamangitsa mayiyo pakhomopo. Pakadali pano anthu ena alangiza mayiyo kuti ngati sakumufunadi mwamuna wakeyo ndi bwino adzingopita kwawo ku Thyolo poopa kuti mwamuna wakeyo angamuchite chipongwe.

22
July

Gulu la mayi ena mu mzinda wa Blantyre likuganiza zokhaulitsa nzawo wina yemwe ali nchizolowezi chomangoyenda mosalabadira kuti ali ndi ana. Nkhaniyi ikuti mayiyo ali ndi ana atatu koma onsewo bamboo wake wake. Mayiyo yemwe amachita geni yogulitsa masamba ndi tomato mu msika wina, akuti amati akachoka m’mawa, amafika pakhomopo usiku, ndipo nthawi zambili amasiya anawo opanda chakudya. Kwa nthawi yaitali, anthu oyandikana naye nyumba akhala akuwapatsa chakudya anawo pokumva chisoni kuti ndi ang’ono ang’ono woti sangathe kudzisamalira okha.   Tsiku lina mayi wina pa lainipo anayiyambitsa nkhaniyi pomadandaulira anzake ena pa momwe mayi nzawoyo akulelera ana ake. Apatu amayi ena omwe samadziwa za khalidwe la mayiyo anati mpofunika kumuphunzitsa mayiyo kuti adziwe udindo wake ngati kholo la anawo. Amayiwo agwirizana kuti tsiku lina adzawatenge anawo nkukawabisa pa khomo lina kuti awone zomwe achite mayi nzawoyo. Amayiwo ati akadzawafunsa za ana akewo mpomwe adzamuuze nkhawa zawo kuti mwina asinthe khalidwe lakelo. Pakadali pano gulu la amayiwo lati lakonzeka kumenyera ufulu wa anawo wolandira chisamaliro cha mayi awo.

22
July

Mwambo wa maliro unasokonekera m’dera la Mfumu Kwataine mboma la Ntcheu chifukwa cha njuchi zomwe zinabalalitsa anthu ku manda. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munachitka maliro a munthu wina odziwika bwino ndipo monga mwa mwambo anthu anasonkhana pa nyumba ya siwa. Pa tsiku loika malirowo, adzukulu analawira kokumba manda ndipo atamaliza ntchitoyo anatumiza uthenga kumudzi. Mwambo wakukhomo unayenda bwino lomwe mpaka anthu kunyamula zovutazo ulendo wakumanda. Koma mwambo uli mkati kumandako, njuchi zomwe sizinaoneke komwe zachokera, zinayamba kubalalitsa anthuwo ndipo akuti ambili mwa iwo anavulala pothawa komanso ena kulumidwa ndi njuchizo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati panatenga nthawi yaitali njuchizo zikuulukabe kumandako ndipo apa mikoko yogona itagundana mitu, inangoganiza zokaika malirowo pakhomo pa mkuluyo. Pamenepa amuna ena olimba mtima anavala zodziteteza mnthupi kuti asalumidwe ndi njuchizo, nkukatenga bokosi la malirowo kubwelera nalo kumudzi. Kunyumbako, mwambo woika m‘mada malemuyo unayenda bwino lomwe popanda chovuta zomwe zachititsa kuti anthu ena aganizire malemuyo kuti anali wokhwima.

22
July

AKUMBUKIRA BANJA LAKE LAKALE

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 191 times

Mai wina kwa gulupu Chipoyola mdera la mfumu Khonsolo mboma la Mzimba waimitsa mitu mikoko yogona chifukwa cha khalidwe lake losintha amuna ngati Malaya.  Nkhaniyi ikuyi mayiyo anali pa banja lolozeka koma masiku apitawa anamuthawa mwamunayo nkukalowelera chikhwaya china m’dera lomwelo.  Mwamuna wakeyo atatsala, naye anapeza mkazi wina ndipo banjalo limakhala bwino lomwe. Patapita nthawi, banja la mayiyo linasokonekera kwa mwamuna anamulowelerayo ndipo apa anakumbukira mwamuna wake wakaleyo.   Pamenepa anauyamba ulendo wakwa mwamuna wake oyambayo koma anaona ngati kutulo atapeza mkazi nzake kunyumbako.  Mayiyo akuti ataona nzakeyo anachita ngati wapenga chifukwa anayamba kuphwanya zinthu pakhomopo ndipo kenaka ndeu inayambika pakati pa amayi awiriwo.  Pa ndeuyo mwini khomolo amachepera mphamvu ndipo apa sanachitire mwina koma kunyanyala banjalo.  Atakasinkhasinkha kwawo, ananyamuka ulendo kwa mwamuna wakeyo komwe anagofikira kuchita nkhondo ndi mkazi nzakeyo.  Chodabwitsa nchoti mwamunayo anayamba kuyikira kumbuyo mkazi wake oyamba anamuthawayo ndipo izi zinadabwitsa anthu ambili.  Pakadali pano mayiyo wabweleranso kwawo koma nzokaikitsa ngati mkazi anamuthawa mwamunayo akhazikike ku banjako.

Page 1 of 152

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter